HEKOLABASI KAPENA PULANETI YOFIIRA
Buku la mtundu wa anthu
Buku laulere

Ndikunenetsa kuti zomwe ndikuyankhula m’bukuli ndi ulosi umene utakwaniritsidwe posachedwapa, chifukwa ndikutsimikiza za kutha kwa dziko lapansili. Zimenezi ndikuzidziwa bwino. Sindikuopseza, koma ndikuchenjeza, chifukwa ndilikuumvera chisoni Mtundu wa anthu osaukawu. Sipapita nthawi yayitali kuti zimenezi zichitike choncho, sipakufunika kutaya nthawi ndi zinthu zomwe si zenizeni. - V.M. Rabolu

M’mbali zonse za dziko lapansi tikupezamo miyambo ndi maulosi okhudza masiku otsiriza, ndipo maulosi onsewa akumafanana.

Ambiri mwa maulosiwa akutichenjeza za zionongeko zazikulu pa dziko lapansili monga kusuntha ndi kutembenuzika kwa dziko lapansi, kusungunuka kwa madzi oundana (ice caps) padzikoli ndi kuzimirira kwa nthaka m’madera akulu akulu adziko lapansili kaamba ka zivomezi zamphamvu ndi ma tsunami.

Pali maulosi osawerengeka amene akunena za chinthu chimodzi chofanana: inde, akunena kweni-kweni za kuyandikira kwa pulaneti yayikulu kwambiri yomwe imafika nkutiyandikira mu kupita kwa nthawi. Pulaneti imeneyo inafikapo kale mu Solar System yathuyi m’mbuyomu ndi kubweretsa chionongeko chomwe chinafafaniza Madera a Lemuria ndi Atilantisi pamodzi ndi zitukuko zawo. Tsopano ifikanso kudzaononga dziko lathuli ndi zitukuko zake ndi kuyambitsa m’badwo ndi nthawi zina zatsopano.

Pulanetiyi ikudziwika mu mbiri, m’maulosi ndi m’mabuku opatulika ndi mayina osiyana-siyana monga: Baal, Pulaneti yozizira, Pulaneti yofiira, Chowawitsa, Ajenjo, Hekolabasi, Barnad I, ndi ena ambiri. Tikunena pano pulaneti imeneyi yayamba kale kuoneka pa makina a telesikopu ndipo kukula kwake ndi pafupifupi kasanu nkamodzi kuposa Jupita.

Mkubwera ndi kupita kwa moyo, chilichonse chimabwerera ku chiyambi kapena chimaliziro chake. Apa ndiye kuti m’mbuyomu, Hekolabasi anathetsa dera la Atilantisi ndi chitukuko chake. Mfundo zimenezi zikugwirizana kwambiri ndi ‘Zigumula Za Dziko Lonse’ zimene zipembedzo ndi zikhalidwe zambiri zimaphunzitsa.

Anthu ambiri anayankhulapo za chinthu chokhudza dziko lonsechi. M’modzi wa iwo ndi V.M. Rabolu, yemwe anafufuza za kuyandikira kwa pulanetiyi kudzera mu ntchito yake ya chitsitsimutso cha chikumbumtima, imene inamuthandiza kuchita kafukufuku wokhudza pulanetiyo. Mu buku lake lotchedwa ‘Hekolabasi kapena Pulaneti Yofiira’, limene likutumizidwa mwaulere pa dziko lapansi ndi a Alcione Association, akuti:

‘Pamene Hekolabasi idzafika kufupi ndi dziko lapansili ndi kukhala mondandana ndi dzuwa, mililri yaoopsa idzayamba kufala padziko lonse lapansi. Palibe dokotala kapena wasayansi yemwe adzadziwe mtundu wa matendawo kapena kuchiritsa kwake. Sadzakhala ndi mphamvu pa miliriyi.’

‘Nthawi yowawitsa ndi yamdima idzafika; kugwedezeka kwa dziko, zivomezi ndi mafunde aakulu pa nyanja. Mitu ya anthu siizidzaganiza bwino chifukwa chosadya ndi kusagona. Sadzaopa zoopsa, azadziponya pansi kuchokera pamalo okwera kwambiri. Misala yeniyeni.’

V.M. Rabolu

V.M. Rabolu, mfufuzi wamkulu wa zophiphiritsa wa ku Colombia, anakweza mawu akekuchenjeza za chiopsezochi. Wanenapo mwatchutchutchu kuti, ibweretsa chimaliziro cha dziko, zitukuko ndi zikhalidwe zathu. M’buku lake, akuphunzitsa njira zomwe tingachotsere zolakwika kapena zilema zathu zamumtima ndinso kulowa mu dera la uzimu ngati njira zokhazo zomwe zilipo kuti tithawe chionongeko chilinkudzachi.

V.M. Rabolu akumaliza ndi mawu akuti: ‘Okondedwa awerengi; ndikunena izi momveka bwino lomwe ndi cholinga chakuti mumvetse kufunika kogwira ntchito yodzilekanitsa ndi ziphena motsimikiza mtima. Aliyense amene akugwira ntchitoyi adzapulumutsidwa ku choopsachi. Izi sizakuti muyikepo maganizo kapena kuzikambirana koma kungozilandira ngati chiphunzitso choona chimene ndachipereka m’bukuli. Palibenso njira ina iliyonse.’

Bungwe La Alcione Association

Bungwe lomwe cholinga chake sikupeza phindu linasankhidwa ngati agent-collaborator mu ntchito yofalitsa ndi kugawa buku la ‘Hekolabasi kapena Pulaneti Yofiira’.

Wolemba: Joaquín Amórtegui Valbuena (V.M. Rabolu)
Wosindikiza: Ángel Prats

Bungwe la Alcione Association linalembetsedwa mu Kaundula wa Mabungwe mu Unduna wa Zam’dziko, gulu 1, ndime 1, nambala 588698, ndipo ili ndi likulu lake ku P.O. Box 4, 09080, m’tauni ya Burgos (Spain)

Zokhudza mlembi

V.M. Rabolu (1926 – 2000)
V.M. Rabolu (1926 – 2000)

V.M. Rabolu (1926 – 2000) anabadwira ku Tolima (Colombia). Mu chaka cha 1952 anapeza Chidziwitso choona ndipo mu zaka zambiri za kuphunzira zophiphiritsa anazama kwambiri pa ntchito yake ndipo anasandulika kukhala mlangizi wa zauzimu wotchuka pa dziko lonse.

Pozindikira za tsogolo lomwe likutiyembekeza, anadzipereka pophunzitsa mtundu wa anthu njira zakubadwanso mwa uzimu. Ndiye kuti, mu zaka za m’ma 1970 anayamba chintchito cholemetsa chophunzitsa athu poyera mosadzikonda za nzeru yoona. Amaphunzitsa anthu maso ndi maso, pochititsa maphunziro ndinso pochitsa misonkhano m’maiko osiyana-siyana.

Mu chaka cha 1998 analemba buku la ‘Hekolabasi kapena Pulaneti Yofiira’. Potengera zomwe iye anaona, V.M. Rabolu akufotokozera zoopsa zomwe zidzachitike pa dziko lathuli posachedwapa ndipo akupereka njira yomwe munthu aliyense anagatsate kuti apeze kusinthika kozama kwa m’moyo mwake. Masiku ano zolembedwa za m’buku lake zikudziwika ndi awerengi ochuluka omwe apindula ndi chiphunzitso chake m’maiko oposa 80.

V.M. Rabolu anali m’modzi wa anthu ochepa kwambiri omwe anali ndi chikumbumtima chotsitsimuka. Ziphunzitso zake ndizofunika kwambiri mu nthawi ino pamene dyera ndi kusalemekezana zafika posonyeza kuti anthu alinkusocherera-socherera.

‘Sindine wodzetsa mantha, ndine munthu wochenjeza za zomwe zilinkudza ndipo zidzachitika.’

V.M. Rabolu

Mawu onenerera

Mu gawo lino, mukhonza kumvera V.M. Rabolu akutchula mawu onenera (mantras) othandiza kuti mulowe m’malo auzimu, ndicholinga chakuti mudziwe katchulidwe kake kolondola.

FA RA ON

LA RA S

Gwirani ntchito limodzi ndi Alcione Association

Bungwe la Alcione Association linakhazikitsidwa motsata malamulo. Monga bungwe lomwe cholinga chake sikupeza phindu, ntchito zake zonse zimachitika mosadzikonda ndi mosafuna phindu lililonse pachuma.

Bungweli limagwira ntchito ngati agent-collaborator wa Bambo Angel Prats, msindikizi wa buku la ‘Hekolabasi kapena Pulaneti Yofiira’; choncho cholinga chake chokhacho ndicho kufalitsa ndi kugawa bukuli pa dziko lonse lapansi. Pa chifukwa chimenechi, ntchito yaikulu ya Alcione Association ndiyotumiza mabuku aulere kulikonse pa dziko lapansi ndi cholinga chofuna kuyesayesa kufalitsa ntchitoyi ndi uthenga wadziko lonsewu kwa aliyense yemwe ali ndi chidwi mosakondera.

Panopa, ntchito yogawayi yalola zikwi zikwi za awerengi kulandira kudzera pa positi buku laulere la ‘Hekolabasi kapena Pulaneti yofiira’. Pofikana lero komanso tsiku ndi tsiku chiwerengero cha opempha bukuli chikunka chikulira-kulira. Chifukwa chakupambana kwakukuluku, tatsimikiza mtima kupitiriza ntchito yogawa bukuli.

Chonde tithandizeni kufalitsa za uthengawu pochita download document ya powerpoint yotsatirayi ndi kuyitumiza kwa anzanu ndi onse omwe mumadziwana nawo.

Ngati mukufuna kulumikizana ndi Bungwe lathuli kapena muli ndi chidwi chofuna kugwira ntchito limodzi ndi wosindikiza pankhani yofuna kufalitsa buku la V.M. Rabolu ndi uthenga uli m”bukuli, kapena kukhala mumgwirizano wamphamvu ndi ife, mukhonza kulembera ku imodzi mwa adilesi izi:

Pa email ku: [email protected]

Pa kalata lemberani ku:
Asociación Alcione
P.O. Box 4, 09080 Burgos (Spain)

Buku laulere

Fomu ya oda

Minda yodziwika ndi asterisk (*) imafunika kuti umalize. Izi zimasonkhanitsidwa ndikugwiritsidwa ntchito pokhapokha kuyankha pempho lanu la buku.

Kuti mulandire bukuli, muyenera kulemba adilesi yoyenera ya imelo.

Kuti mumalize pempho lanu, werengani ndikuyang’ana bokosilo.

Mwa kuwonekera pa batani la Tumiza, mumavomereza kusanthula kwa datazo malinga ndi, ndipo pazolinga zomwe zalembedwa, Mfundo Zachinsinsi.

Alcyone Association